Yesaya 13:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 “Taonani! Tsiku la Yehova likubwera. Tsikulo n’lankhanza, laukali ndiponso lamkwiyo woyaka moto. Likubwera kuti lidzachititse dziko kukhala chinthu chodabwitsa,+ ndiponso kuti lidzawononge anthu ochimwa a m’dzikolo.+ Yesaya 27:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Tinthambi take tikadzauma, akazi obwera kumeneko adzatithyola n’kutiyatsa.+ Pakuti anthuwo si omvetsa zinthu.+ N’chifukwa chake yemwe anawapanga sadzawachitira chifundo, ndipo yemwe anawaumba sadzawakomera mtima.+ Ezekieli 7:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Diso langa silidzakumvera chisoni+ ndipo sindidzakuchitira chifundo. Ine ndidzakubwezera mogwirizana ndi njira zako, ndipo ukamadzalangidwa udzaona zotsatirapo za zinthu zako zonyansa zimene zili pakati pako.+ Chotero anthu inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.’+ Ezekieli 24:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Tsoka lako lidzabwera ndithu+ ndipo ndidzachitapo kanthu. Sindidzazengereza,+ kumva chisoni+ kapena kusintha maganizo.+ Iwo adzakuweruza mogwirizana ndi njira zako ndi zochita zako.+ Ine Yehova ndanena,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.” Aroma 2:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Koma chifukwa chakuti ndiwe wosafuna kusintha khalidwe+ ndiponso wa mtima wosalapa,+ ukudzisungira mkwiyo wa Mulungu.+ Mulungu adzasonyeza mkwiyo+ umenewu pa tsiku loulula+ chiweruzo chake cholungama.+
9 “Taonani! Tsiku la Yehova likubwera. Tsikulo n’lankhanza, laukali ndiponso lamkwiyo woyaka moto. Likubwera kuti lidzachititse dziko kukhala chinthu chodabwitsa,+ ndiponso kuti lidzawononge anthu ochimwa a m’dzikolo.+
11 Tinthambi take tikadzauma, akazi obwera kumeneko adzatithyola n’kutiyatsa.+ Pakuti anthuwo si omvetsa zinthu.+ N’chifukwa chake yemwe anawapanga sadzawachitira chifundo, ndipo yemwe anawaumba sadzawakomera mtima.+
4 Diso langa silidzakumvera chisoni+ ndipo sindidzakuchitira chifundo. Ine ndidzakubwezera mogwirizana ndi njira zako, ndipo ukamadzalangidwa udzaona zotsatirapo za zinthu zako zonyansa zimene zili pakati pako.+ Chotero anthu inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.’+
14 Tsoka lako lidzabwera ndithu+ ndipo ndidzachitapo kanthu. Sindidzazengereza,+ kumva chisoni+ kapena kusintha maganizo.+ Iwo adzakuweruza mogwirizana ndi njira zako ndi zochita zako.+ Ine Yehova ndanena,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”
5 Koma chifukwa chakuti ndiwe wosafuna kusintha khalidwe+ ndiponso wa mtima wosalapa,+ ukudzisungira mkwiyo wa Mulungu.+ Mulungu adzasonyeza mkwiyo+ umenewu pa tsiku loulula+ chiweruzo chake cholungama.+