Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 30:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Yehova Mulungu wanu adzabweza kwawo anthu a mtundu wanu amene anagwidwa ndi kupita kudziko lina,+ ndipo adzakumverani chifundo+ n’kukusonkhanitsaninso pamodzi kuchokera pakati pa anthu onse kumene Yehova Mulungu wanu anakubalalitsirani.+

  • Yeremiya 3:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 “M’masiku amenewo nyumba ya Yuda idzayenda pamodzi ndi nyumba ya Isiraeli,+ ndipo onse+ adzatuluka m’dziko la kumpoto ndi kulowa m’dziko limene ndinapereka kwa makolo anu monga cholowa chawo.+

  • Yeremiya 24:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Maso anga adzakhala pa iwo kuti ndiwachitire zabwino,+ ndipo ndidzawabwezeretsa kudziko lino.+ Pamenepo ndidzawalimbitsa, osati kuwapasula. Ndidzawabzala, osati kuwazula.+

  • Yeremiya 30:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Pakuti, “taona! masiku adzafika,” watero Yehova, “pamene ndidzasonkhanitsa Isiraeli ndi Yuda,+ anthu anga amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina,” watero Yehova. “Iwo ndidzawabwezeretsa kudziko limene ndinapatsa makolo awo ndipo adzalitenga kukhalanso lawo.”’”+

  • Yeremiya 32:37
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 37 ‘Inetu ndikuwasonkhanitsa pamodzi kuchokera kumayiko onse kumene ndinawabalalitsira nditakwiya, kupsa mtima ndiponso ndili ndi ukali waukulu.+ Ndidzawabwezeretsa m’dziko lino ndi kuwachititsa kukhala mwamtendere.+

  • Amosi 9:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Pamenepo ndidzasonkhanitsa ndi kubwezeretsa anthu anga Aisiraeli amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita ku ukapolo.+ Iwo adzamanga mizinda imene ili yabwinja ndi kukhalamo.+ Adzalima minda ya mpesa ndi kumwa vinyo wochokera m’mindayo. Adzalimanso minda ya zipatso ndi kudya zipatso zochokera m’mindayo.’+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena