Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Mafumu 9:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Nyumba iyi idzakhala bwinja.+ Aliyense wodutsa pafupi nayo adzayang’ana modabwa+ ndi kuimba mluzu n’kunena kuti, ‘N’chifukwa chiyani Yehova anachita zimenezi padzikoli ndi panyumbayi?’+

  • Yeremiya 18:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Choncho dziko lawo lidzakhala chinthu chodabwitsa kwa ena,+ chinthu chimene adzachiimbira mluzu mpaka kalekale.+ Aliyense wodutsa pafupi ndi dzikoli adzaliyang’anitsitsa modabwa ndipo adzapukusa mutu wake.+

  • Yeremiya 19:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Ndidzasandutsa mzindawu kukhala chinthu chodabwitsa kwa ena, chimene azidzachiimbira mluzu.+ Aliyense wodutsa pafupi nawo adzauyang’anitsitsa modabwa ndipo adzaulizira mluzu chifukwa cha miliri yake yonse.+

  • Yeremiya 25:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 ndikuitana mafuko onse akumpoto,”+ watero Yehova, “ndipo ndikuitananso Nebukadirezara mfumu ya Babulo, mtumiki wanga.+ Ndikuitana anthu amenewa kuti aukire dziko lino+ ndi anthu okhala mmenemo, komanso kuti aukire mitundu yonse yokuzungulirani.+ Ndidzakuwonongani inuyo ndi mitundu yonse yokuzungulirani, ndi kukusandutsani chinthu chodabwitsa chimene azidzachiimbira mluzu+ ndipo malo anu adzakhala mabwinja mpaka kalekale.+

  • Mika 6:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Anthu inu mukutsatira zochita za Omuri.+ Zochita zonse za anthu a nyumba ya Ahabu, inunso mukuzichita+ ndipo mukuyendera maganizo awo.+ Pa chifukwa chimenechi ndidzakusandutsani chinthu chodabwitsa ndipo anthu a mumzindawo adzakhala oyenera kuwaimbira mluzu.+ Inuyo mudzatonzedwa ndi mitundu ina ya anthu.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena