Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 28:37
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 37 Pamenepo udzakhala chodabwitsa,+ adzakupekera mwambi+ ndi kukutonza pakati pa mitundu yonse ya anthu amene Yehova adzakupititsako.

  • 1 Mafumu 9:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 ineyo ndidzachotsa Aisiraeli padziko limene ndawapatsa+ ndipo nyumba imene ndaiyeretsa ndi dzina langa, ndidzaichotsa pamaso panga.+ Aisiraeli adzawapekera mwambi+ ndi kuwatonza pakati pa mitundu yonse ya anthu.

  • 2 Mbiri 7:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 ineyo ndidzakuchotsani padziko langa limene ndakupatsani+ ndipo nyumba iyi yomwe ndaiyeretsa+ chifukwa cha dzina langa, ndidzaichotsa pamaso panga.+ Ndidzachititsa anthu kuipekera mwambi+ ndi kuitonza pakati pa mitundu yonse ya anthu.+

  • Salimo 79:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Anthu oyandikana nafe akutitonza,+

      Anthu otizungulira akutinyoza ndi kutiseka.+

  • Salimo 80:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  6 Mwachititsa kuti anthu oyandikana nafe azimenyana polimbirana ifeyo.+

      Ndipo adani athu akupitirizabe kutinyoza mmene akufunira.+

  • Yeremiya 18:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Choncho dziko lawo lidzakhala chinthu chodabwitsa kwa ena,+ chinthu chimene adzachiimbira mluzu mpaka kalekale.+ Aliyense wodutsa pafupi ndi dzikoli adzaliyang’anitsitsa modabwa ndipo adzapukusa mutu wake.+

  • Ezekieli 5:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 “‘Iweyo ndidzakusandutsa malo abwinja. Ndidzakusandutsanso chitonzo pakati pa mitundu yokuzungulira ndi pamaso pa munthu aliyense wodutsa.+

  • Ezekieli 23:32
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 32 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Udzamwa za m’kapu ya mkulu wako, kapu yaitali ndi yaikulu.+ Udzakhala chinthu choseketsa ndi chotonzedwa chifukwa m’kapumo muli zambiri.+

  • Danieli 9:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Inu Yehova, nthawi zonse mumachita zinthu zolungama.+ Chonde, chotsani mkwiyo wanu waukulu pa Yerusalemu, phiri lanu loyera.+ Pakuti chifukwa cha machimo athu ndi zolakwa za makolo athu,+ Yerusalemu ndi anthu anu takhala chinthu chotonzedwa ndi anthu onse otizungulira.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena