8 “‘Ndinadutsa pafupi nawe n’kukuona, ndipo ndinaona kuti inali nthawi yako yoti uchite zachikondi.+ Chotero ndinakuphimba ndi chovala changa+ ndipo ndinabisa maliseche ako. Ndinakulumbirira n’kuchita nawe pangano+ ndipo unakhala wanga,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.