1 Mafumu 22:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Choncho Mikaya anati: “Ndikuona Aisiraeli onse atabalalika+ m’mapiri ngati nkhosa zopanda m’busa.+ Ndipo Yehova anati: ‘Amenewa alibe atsogoleri. Aliyense abwerere kunyumba kwake mu mtendere.’”+ Yeremiya 23:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Yehova Mulungu wa Isiraeli wadzudzula abusa amene akuweta anthu ake kuti: “Inu mwabalalitsa nkhosa zanga. Mukupitiriza kuzimwaza ndipo simukuzisamalira.”+ “Tsopano ndikutembenukira kwa inu chifukwa cha zochita zanu zoipazo,”+ watero Yehova. Yeremiya 50:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Anthu anga akhala ngati gulu la nkhosa zosakazidwa.+ Abusa awo awayendetsa uku ndi uku.+ Awayendetsa uku ndi uku m’mapiri popanda cholinga.+ Awachotsa paphiri ndi chitunda china kupita paphiri ndi chitunda china. Iwo aiwala malo awo ampumulo.+ Mateyu 9:36 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 36 Poona chikhamu cha anthu, iye anawamvera chisoni,+ chifukwa anali onyukanyuka ndi otayika ngati nkhosa zopanda m’busa.+ Maliko 6:34 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 34 Koma potsika, anaona khamu lalikulu la anthu, ndipo anawamvera chifundo,+ chifukwa anali ngati nkhosa zopanda m’busa.+ Choncho anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.+
17 Choncho Mikaya anati: “Ndikuona Aisiraeli onse atabalalika+ m’mapiri ngati nkhosa zopanda m’busa.+ Ndipo Yehova anati: ‘Amenewa alibe atsogoleri. Aliyense abwerere kunyumba kwake mu mtendere.’”+
2 Yehova Mulungu wa Isiraeli wadzudzula abusa amene akuweta anthu ake kuti: “Inu mwabalalitsa nkhosa zanga. Mukupitiriza kuzimwaza ndipo simukuzisamalira.”+ “Tsopano ndikutembenukira kwa inu chifukwa cha zochita zanu zoipazo,”+ watero Yehova.
6 Anthu anga akhala ngati gulu la nkhosa zosakazidwa.+ Abusa awo awayendetsa uku ndi uku.+ Awayendetsa uku ndi uku m’mapiri popanda cholinga.+ Awachotsa paphiri ndi chitunda china kupita paphiri ndi chitunda china. Iwo aiwala malo awo ampumulo.+
36 Poona chikhamu cha anthu, iye anawamvera chisoni,+ chifukwa anali onyukanyuka ndi otayika ngati nkhosa zopanda m’busa.+
34 Koma potsika, anaona khamu lalikulu la anthu, ndipo anawamvera chifundo,+ chifukwa anali ngati nkhosa zopanda m’busa.+ Choncho anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.+