-
Yesaya 3:24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 “Ndiyeno chidzachitike n’chakuti, m’malo mwa mafuta a basamu onunkhira+ padzangokhala fungo loipa, m’malo mwa lamba padzakhala chingwe, m’malo mwa tsitsi lokonzedwa bwino padzakhala mpala,+ m’malo mwa chovala chamtengo wapatali munthu adzavala chiguduli,*+ ndipo padzakhala chipsera*+ m’malo mwa kukongola.
-
-
Amosi 8:10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Ndidzasandutsa zikondwerero zanu kukhala maliro+ ndipo nyimbo zanu zonse zidzakhala nyimbo zoimba polira. Ndidzachititsa kuti anthu onse avale ziguduli* ndipo mitu yonse idzametedwa mpala.+ Ndidzachititsa kuti zochitika pa tsikulo zikhale ngati maliro a mwana wamwamuna mmodzi yekhayo amene wamwalira,+ moti tsiku la mapeto a zinthu zonsezi lidzakhala lowawa.’
-