-
2 Mbiri 7:3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Ana onse a Isiraeli anali kuonerera pamene moto unali kutsika, ndiponso pamene ulemerero wa Yehova unaonekera pamwamba pa nyumbayo. Ataona zimenezi, nthawi yomweyo anagwada+ n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi+ ndi kuyamika Yehova, “chifukwa iye ndi wabwino,+ pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhala mpaka kalekale.”+
-
-
Ezekieli 1:28Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
28 Panali chinachake chooneka ngati utawaleza+ umene umaoneka mumtambo pa tsiku la mvula yamphamvu. Umu ndi mmene kuwala kozungulira pamalopo kunali kuonekera. Zinali kuoneka ngati ulemerero wa Yehova.+ Nditaona zimenezo, ndinagwada n’kuwerama mpaka nkhope yanga pansi.+ Kenako ndinayamba kumva mawu a winawake akulankhula.
-