Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 18:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Pakati panu pasapezeke munthu wotentha mwana wake pamoto,*+ wolosera,+ wochita zamatsenga,+ woombeza,*+ wanyanga,+

  • Deuteronomo 18:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 “Mitundu imene ukuilanda dziko inali kumvera anthu ochita zamatsenga+ ndi olosera.+ Koma iwe, Yehova Mulungu wako sanakulole kuchita zimenezi.+

  • Yesaya 44:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Ndimalepheretsa zizindikiro za anthu olankhula zinthu zopanda pake, ndipo ndine amene ndimachititsa olosera kuchita zamisala.+ Ndine amene ndimachititsa anthu anzeru kubwerera kumbuyo, ndiponso amene ndimachititsa nzeru zawo kukhala zopusa.+

  • Yeremiya 27:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 “‘“‘Anthu inu musamvere aneneri,+ ochita zamaula, olota maloto,+ ochita zamatsenga ndi obwebweta+ amene ali pakati panu ndipo akukuuzani kuti: “Anthu inu simudzatumikira mfumu ya Babulo.”+

  • Ezekieli 12:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Pakati pa nyumba ya Isiraeli sipadzakhalanso masomphenya opanda pake+ kapena kulosera kwachiphamaso.+

  • Mika 3:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 ‘Choncho anthu inu usiku udzakufikirani,+ ndipo simudzaonanso masomphenya.+ Mudzangoona mdima wokhawokha moti simudzaloseranso. Aneneri amenewa dzuwa lidzawalowera ndipo mdima udzawagwera masanasana.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena