23 Ahaziyo anayamba kupereka nsembe kwa milungu+ ya ku Damasiko+ imene inali kumuukira, ndipo anati: “Chifukwa chakuti milungu ya mafumu a Siriya ikuwathandiza,+ ndipereka nsembe kwa iyo kuti inenso indithandize.”+ Koma milunguyo inakhala chopunthwitsa kwa iye ndi kwa Aisiraeli onse.+