7 Chotero Ahazi anatumiza amithenga kwa Tigilati-pilesere+ mfumu ya Asuri ndi uthenga wakuti: “Ndine mtumiki wanu+ ndi mwana wanu. Bwerani mudzandipulumutse+ m’manja mwa mfumu ya Siriya ndi m’manja mwa mfumu ya Isiraeli, amene akundiukira.”
18 Ndiyeno n’chifukwa chiyani ukufuna kuyenda m’njira ya ku Iguputo+ kuti ukamwe madzi a mumtsinje wa Sihori?+ N’chifukwa chiyani ukufuna kuyenda m’njira yopita kudziko la Asuri+ kuti ukamwe madzi a mumtsinje wa Firate?