-
Yesaya 31:1Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
31 Tsoka kwa anthu amene akupita ku Iguputo kukapempha thandizo.+ Iwo akudalira mahatchi wamba+ ndi kukhulupirira magaleta ankhondo,+ chifukwa chakuti ndi ambiri. Akudaliranso mahatchi akuluakulu chifukwa chakuti ndi amphamvu kwambiri, koma sanayang’ane kwa Woyera wa Isiraeli ndipo sanafunefune Yehova.+
-