Ekisodo 34:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Kenako iye anati: “Tsopano ngati mwandikomera mtima, inu Yehova, chonde, Yehova ayende nafe pakati pathu,+ chifukwa anthuwa ndi ouma khosi,+ ndipo mutikhululukire zolakwa zathu ndi machimo athu,+ ndi kutitenga kukhala chuma chanu.”+ Nehemiya 9:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 “Koma iwo, makolo athu, anachita zinthu modzikuza+ moti anaumitsa khosi lawo+ ndipo sanamvere malamulo anu. Yeremiya 3:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Choncho mvula yamvumbi yasiya kugwa,+ ndipo mvula yomalizira siinagwe.+ Ukuchita zinthu mopanda manyazi ngati mkazi amene akuchita uhule.* Palibe chimene chikukuchititsa manyazi.+ Yeremiya 5:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Inu Yehova, kodi maso anu sakulakalaka kuona munthu wokhulupirika?+ Mwawalanga+ koma sanamve kupweteka.+ Ngakhale kuti munatsala pang’ono kuwafafaniza onse,+ iwo sanaphunzirepo* kanthu.+ Anaumitsa nkhope zawo ngati thanthwe.+ Ndipo anakana kubwerera kwa inu.+ Yeremiya 7:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 Koma iwo sanandimvere kapena kutchera khutu lawo.+ M’malomwake anapitiriza kuumitsa khosi lawo,+ ndipo anachita zinthu zoipa kuposa makolo awo.+ Ezekieli 2:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Ndikukutumiza kwa ana a nkhope zamwano+ ndi amakani,*+ ndipo ukawauze kuti, ‘Izi n’zimene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena.’
9 Kenako iye anati: “Tsopano ngati mwandikomera mtima, inu Yehova, chonde, Yehova ayende nafe pakati pathu,+ chifukwa anthuwa ndi ouma khosi,+ ndipo mutikhululukire zolakwa zathu ndi machimo athu,+ ndi kutitenga kukhala chuma chanu.”+
16 “Koma iwo, makolo athu, anachita zinthu modzikuza+ moti anaumitsa khosi lawo+ ndipo sanamvere malamulo anu.
3 Choncho mvula yamvumbi yasiya kugwa,+ ndipo mvula yomalizira siinagwe.+ Ukuchita zinthu mopanda manyazi ngati mkazi amene akuchita uhule.* Palibe chimene chikukuchititsa manyazi.+
3 Inu Yehova, kodi maso anu sakulakalaka kuona munthu wokhulupirika?+ Mwawalanga+ koma sanamve kupweteka.+ Ngakhale kuti munatsala pang’ono kuwafafaniza onse,+ iwo sanaphunzirepo* kanthu.+ Anaumitsa nkhope zawo ngati thanthwe.+ Ndipo anakana kubwerera kwa inu.+
26 Koma iwo sanandimvere kapena kutchera khutu lawo.+ M’malomwake anapitiriza kuumitsa khosi lawo,+ ndipo anachita zinthu zoipa kuposa makolo awo.+
4 Ndikukutumiza kwa ana a nkhope zamwano+ ndi amakani,*+ ndipo ukawauze kuti, ‘Izi n’zimene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena.’