9 Ngakhalenso m’mitima mwathu, tinali kumva ngati talandira chiweruzo cha imfa. Zinatero kuti tisakhale ndi chikhulupiriro mwa ife tokha,+ koma mwa Mulungu amene amaukitsa akufa.+
6 Ndiponso, popanda chikhulupiriro+ n’zosatheka kukondweretsa Mulungu.+ Pakuti aliyense wofika kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti iye alikodi,+ ndi kuti amapereka mphoto+ kwa anthu omufunafuna ndi mtima wonse.+