Hoseya 9:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 “Zoipa zawo zonse zinachitikira ku Giligala,+ ndipo ndinadana nawo kwambiri kumeneko.+ Chifukwa cha zochita zawo zoipa, ndidzawathamangitsa panyumba yanga.+ Sindidzapitiriza kuwakonda.+ Akalonga awo onse akuchita makani.+ Hoseya 12:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 “Ku Giliyadi anthu akuchita zamatsenga+ ndiponso akulankhula zabodza.+ Ku Giligala akupereka nsembe ng’ombe zamphongo.+ Komanso maguwa awo ansembe ali ngati milu ya miyala m’mizere ya m’munda.+ Amosi 4:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 “‘Bwerani ku Beteli anthu inu kuti mudzachite zolakwa.+ Muzichita zolakwa mobwerezabwereza ku Giligala+ ndipo muzibweretsa nsembe zanu m’mawa. Pa tsiku lachitatu, muzibweretsa chakhumi* chanu.+
15 “Zoipa zawo zonse zinachitikira ku Giligala,+ ndipo ndinadana nawo kwambiri kumeneko.+ Chifukwa cha zochita zawo zoipa, ndidzawathamangitsa panyumba yanga.+ Sindidzapitiriza kuwakonda.+ Akalonga awo onse akuchita makani.+
11 “Ku Giliyadi anthu akuchita zamatsenga+ ndiponso akulankhula zabodza.+ Ku Giligala akupereka nsembe ng’ombe zamphongo.+ Komanso maguwa awo ansembe ali ngati milu ya miyala m’mizere ya m’munda.+
4 “‘Bwerani ku Beteli anthu inu kuti mudzachite zolakwa.+ Muzichita zolakwa mobwerezabwereza ku Giligala+ ndipo muzibweretsa nsembe zanu m’mawa. Pa tsiku lachitatu, muzibweretsa chakhumi* chanu.+