Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 22:32
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 32 Musaipitse dzina langa loyera,+ m’malomwake muzindiona kukhala wopatulika pakati pa ana a Isiraeli.+ Ine ndine Yehova amene ndikukupatulani kuti mukhale oyera.+

  • Deuteronomo 32:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  3 Pakuti ndidzalengeza dzina la Yehova.+

      Vomerezani ukulu wa Mulungu wathu!+

  • Salimo 145:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Pakamwa panga padzalankhula zotamanda Yehova,+

      Ndipo anthu onse atamande dzina lake loyera mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.+

  • Yesaya 5:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Yehova wa makamu adzakwezeka kudzera m’chiweruzo,+ ndipo Mulungu woona, Woyera,+ adzadziyeretsa kudzera m’chilungamo.+

  • Yesaya 8:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Yehova wa makamu ndi amene muyenera kumuona kuti ndi woyera,+ ndipo iyeyo ndi amene muyenera kumuopa.+ Iye ndi amene ayenera kukuchititsani kunjenjemera.”+

  • Yesaya 29:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 pakuti akaona ana ake pakati pake, ntchito ya manja anga,+ iwo adzayeretsa dzina langa.+ Adzayeretsadi Woyera wa Yakobo,+ ndipo adzalemekeza kwambiri Mulungu wa Isiraeli.+

  • Ezekieli 36:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 ‘Ndidzayeretsa dzina langa lalikulu+ limene linali kudetsedwa pakati pa mitundu ina ya anthu. Inu munadetsa dzina langalo pakati pa anthu a mitundu ina. Ndikadzayeretsedwa pakati panu, pamaso pa anthu a mitundu inawo, iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena