6 Koma Khristu monga Mwana+ wa mwiniwake wa nyumbayo, anali kuyang’anira nyumba ya Mulungu mokhulupirika. Ife ndife nyumba ya Mulunguyo,+ ngati tagwira mwamphamvu ufulu wathu wa kulankhula ndi kupitirizabe kunyadira chiyembekezocho mpaka mapeto.+
6 Wodala+ ndi woyera+ ndiye aliyense wouka nawo pa kuuka koyamba. Pa iwo, imfa yachiwiri+ ilibe ulamuliro.+ Koma adzakhala ansembe+ a Mulungu ndi a Khristu, ndipo adzalamulira monga mafumu limodzi naye zaka 1,000.+