4 Amene anatsagana naye pa ulendowu anali Sopaturo+ mwana wa Puro wa ku Bereya, Arisitako+ ndi Sekundo a ku Tesalonika, Gayo wa ku Debe, ndi Timoteyo,+ koma ochokera m’chigawo cha Asia anali Tukiko+ ndi Terofimo.+
2 Ku Adiramutiyo tinakwera ngalawa imene inali pafupi kunyamuka ulendo wopita kumalo osiyanasiyana a m’mphepete mwa nyanja m’chigawo cha Asia. Kenako tinanyamuka, tilinso limodzi ndi Arisitako,+ yemwe anali Mmakedoniya wa ku Tesalonika.