30 Pamenepo chizindikiro cha Mwana wa munthu+ chidzaonekera kumwamba. Ndiyeno mafuko onse a padziko lapansi adzadziguguda pachifuwa chifukwa cha chisoni,+ ndipo adzaona Mwana wa munthu akubwera pamitambo ya kumwamba ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.+
10 Pakuti mtima wa aliyense wa ife udzaonekera pamaso pa mpando woweruzira milandu wa Khristu,+ kuti aliyense alandire mphoto yake pa zinthu zimene anachita ali m’thupi, mogwirizana ndi zimene anali kuchita, zabwino kapena zoipa.+
16 Chifukwa Ambuye mwini adzatsika kumwamba,+ ndi mfuu yolamula ya mawu a mkulu wa angelo,+ ndi lipenga+ la Mulungu. Ndipo amene anafa mwa Khristu adzauka choyamba.+