Nyimbo ya Solomo
7 “Mapazi ako akukongola kwambiri munsapato zako,
Iwe mwana wamkazi wolemekezeka.
Ntchafu zako nʼzoumbidwa bwino ngati zinthu zodzikongoletsera,
Ntchito ya manja a munthu waluso.
2 Mchombo wako uli ngati mbale yolowa.
Vinyo wosakaniza bwino asasowepo.
Mimba yako ili ngati mulu wa tirigu,
Wozunguliridwa ndi maluwa.
4 Khosi lako+ lili ngati nsanja ya mnyanga wa njovu.+
Mphuno yako ili ngati nsanja ya ku Lebanoni,
Imene inayangʼana cha ku Damasiko.
5 Mutu wako ndi wokongola ngati phiri la Karimeli,+
Ndipo tsitsi lako lopotanapotana+ lili ngati ubweya wa nkhosa wapepo.+
Mfumu yakopeka* ndi tsitsi lako lalitali lokongolalo.
6 Ndiwe wokongola kwambiri mtsikana iwe ndipo ndiwe wosangalatsa,
Kuposa zinthu zina zonse zimene zimasangalatsa mtima wa munthu.
8 Ine ndinanena kuti, ‘Ndikwera mtengo wa kanjedza
Kuti ndikathyole nthambi zake zokhala ndi zipatso.’
Mabere ako akhale ngati phava la zipatso za mpesa,
Ndipo mpweya wamʼkamwa mwako ununkhire ngati maapozi,
9 Ndipo mʼkamwa mwako mununkhire ngati vinyo wabwino kwambiri.”
“Adutse mwamyaa kukhosi kwa wokondedwa wanga,
Ngati vinyo amene amadutsa mwamyaa pakamwa nʼkuyambitsa tulo kwa amuna.
12 Tiye tilawirire mʼmamawa tipite kuminda ya mpesa.
Tikaone ngati mitengo ya mpesa yaphukira,
Ngati maluwa amasula+
Ngati mitengo ya makangaza yachita maluwa.+
Kumeneko ndikakusonyeza chikondi changa.+
13 Zipatso za mandereki*+ zikununkhira,
Pamakomo olowera kunyumba zathu pali zipatso zosiyanasiyana zokoma kwambiri.+
Ndakusungira zipatso zatsopano ndi zakale zomwe,
Iwe wachikondi wanga.”