MALAKI
1 Uthenga wokhudza Isiraeli:
Awa ndi mawu a Yehova opita kwa Isiraeli kudzera mwa Malaki:*
2 Yehova wanena kuti: “Ine ndimakukondani anthu inu.”+
Koma inu mwanena kuti: “Mwasonyeza bwanji kuti mumatikonda?”
“Kodi Esau sanali mchimwene wake wa Yakobo?+ Koma ine ndinakonda Yakobo,” watero Yehova. 3 “Esau ndinadana naye.+ Mapiri ake ndinawasandutsa bwinja+ ndipo cholowa chake ndinachisandutsa malo okhala mimbulu yamʼchipululu.”+
4 “Ngakhale kuti Edomu akunena kuti, ‘Ife tawonongedwa, koma tibwerera nʼkukamanga malo athu owonongedwawo,’ Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Iwo apita kukamanga, koma ine ndikagwetsa. Anthu adzatchula malo awowo kuti “dera la zoipa” ndipo iwowo adzatchedwa “anthu okanidwa ndi Yehova mpaka kalekale.”+ 5 Inu mudzaona zimenezi ndi maso anu ndipo mudzati: “Yehova atamandike mʼdera lonse la Isiraeli.”’”
6 “‘Mwana amalemekeza bambo ake+ ndipo wantchito amalemekeza mbuye wake. Ngati ine ndili bambo,+ ulemu wanga uli kuti?+ Ngati ndili ambuye,* nʼchifukwa chiyani simundiopa?’* ndikutero ine Yehova wa magulu ankhondo akumwamba kwa inu ansembe amene mukunyoza dzina langa.+
‘Koma inu mukunena kuti: “Kodi dzina lanu talinyoza bwanji?”’
7 ‘Mwalinyoza popereka nsembe* zodetsedwa paguwa langa lansembe.’
‘Inu mukunena kuti: “Takudetsani bwanji?”’
‘Mwandidetsa ponena kuti: “Tebulo la Yehova+ ndi lonyozeka.” 8 Mukapereka nsembe nyama yakhungu, mumanena kuti: “Palibe cholakwika.” Mukapereka nsembe nyama yolumala kapena yodwala, mumati: “Palibe vuto.”’”+
“Pitani nazo kwa bwanamkubwa wanu. Kodi akakondwera nanu? Kapena kodi akakulandirani bwino?” watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.
9 “Tsopano khazikani pansi mtima wa Mulungu kuti achite chifundo. Kodi nsembe zimene mukuperekazi zingachititse kuti ndisangalale nanu?” watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.
10 “Ndipo ndani wa inu amene angatseke zitseko za kachisi popanda malipiro?+ Mukayatsa moto paguwa langa lansembe, mumafuna kulandira malipiro.+ Ine sindikukondwera nanu, ndipo nsembe zimene mukundipatsa ngati mphatso sizikundisangalatsa,”+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.
11 “Kuchokera kotulukira dzuwa kukafika kumene limalowera,* dzina langa lidzakwezeka pakati pa anthu a mitundu ina.+ Kulikonse anthu azidzapereka nsembe zautsi ndiponso nsembe zina ngati mphatso zovomerezeka polemekeza dzina langa. Adzachita izi chifukwa dzina langa lidzakwezeka pakati pa anthu a mitundu inawo,”+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.
12 “Koma inu mukulinyoza*+ ponena kuti, ‘Palibe vuto kudetsa tebulo la Yehova, ndipo zopereka kapena kuti chakudya chimene chili pamenepo nʼchonyozeka.’+ 13 Mumanenanso kuti, ‘Koma ndiye nʼzotopetsa bwanji!’ Ndipo mumanunkhiza nsembezo monyansidwa,” watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. “Inu mumabweretsa nyama zobedwa, zolumala ndi zodwala. Mumabweretsa zimenezi ngati mphatso. Kodi ine ndingalandire nsembe zoterezi?”+ watero Yehova.
14 “Wotembereredwa ndi aliyense wochita zachinyengo, amene ali ndi nyama yabwinobwino yamphongo pa ziweto zake koma amalonjeza nʼkupereka nsembe nyama yachilema kwa Yehova. Ine ndine Mfumu yaikulu+ ndipo dzina langa lidzaopedwa pakati pa anthu a mitundu ina,” watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.+
2 “Tsopano inu ansembe, lamulo ili ndi lanu.+ 2 Mukakana kumvera ndiponso kuganizira nkhani imeneyi mumtima mwanu kuti mulemekeze dzina langa, ndidzakutumizirani temberero+ ndipo madalitso anu ndidzawasandutsa matemberero. Madalitso ndawasandutsa matemberero+ chifukwa nkhani imeneyi simunaiganizire mumtima mwanu,” watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.
3 “Tamverani! Chifukwa cha inu, ndiwononga mbewu zanu zomwe mwadzala+ ndipo ndikuwazani ndowe kumaso. Ndikuwazani ndowe za nyama zimene mumapereka nsembe pa zikondwerero zanu. Ndipo mudzanyamulidwa nʼkukaponyedwa pandowezo.* 4 Zikadzatero mudzadziwa kuti ine ndakupatsani lamulo limeneli kuti pangano limene ndinachita ndi Levi lipitirire,”+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.
5 “Pangano limene ndinachita naye linali loti ndinamupatsa moyo ndi mtendere kuti azindiopa. Iye ankandiopa ndipo ankalemekeza dzina langa. 6 Ankaphunzitsa lamulo la choonadi+ ndipo sanalankhulepo zinthu zoipa. Ankayenda ndi ine mwamtendere komanso mowongoka mtima+ ndipo anabweza anthu ambiri panjira yolakwika. 7 Wansembe ayenera kuphunzitsa anthu za Mulungu. Anthu ayenera kupita kwa iye kuti akamve Chilamulo*+ chifukwa iye ndi mthenga wa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.
8 Koma inu mwasiya kuyenda panjira yoyenera. Mwachititsa kuti anthu ambiri asiye kutsatira Chilamulo.*+ Ndipo mwaphwanya pangano limene ndinachita ndi Levi,”+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. 9 “Choncho ine ndidzachititsa kuti inu mukhale anthu onyozeka ndi otsika kwa anthu onse, chifukwa simunayende mʼnjira zanga, koma munkakondera pa nkhani zokhudza kutsatira Chilamulo.”+
10 “Kodi tonsefe atate wathu si mmodzi?+ Kodi si Mulungu mmodzi amene anatilenga? Ndiye nʼchifukwa chiyani tikuchitirana zachinyengo+ nʼkumaipitsa pangano la makolo athu akale? 11 Yuda wachita zachinyengo, ndipo mu Isiraeli ndi mu Yerusalemu mwachitika zinthu zonyansa. Chifukwa Yuda wadetsa chiyero* cha Yehova+ chimene Mulungu amachikonda, ndipo Yuda wakwatira mwana wamkazi wa mulungu wachilendo.+ 12 Yehova adzapha munthu aliyense wochita zimenezi mʼmatenti a Yakobo, kaya akhale ndani.* Adzachita zimenezi ngakhale zitakhala kuti munthuyo amapereka nsembe ngati mphatso kwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.”+
13 “Pali chinthu chinanso chimene anthu inu mukuchita ndipo chikuchititsa kuti guwa lansembe la Yehova lidzaze ndi misozi, kulira ndi kubuula. Chifukwa cha zimenezi, nsembe zanu zimene mumapereka ngati mphatso nʼzosavomerezeka kwa iye ndipo sakusangalala ndi chilichonse chochokera mʼmanja mwanu.+ 14 Inu mwanena kuti, ‘Chifukwa chiyani?’ Chifukwa chakuti Yehova ndi mboni pakati pa inu ndi mkazi amene munamukwatira muli mnyamata, yemwe mwamuchitira zachinyengo ngakhale kuti iye ndi mnzanu komanso mkazi wa pangano.*+ 15 Komabe pali ena amene sanachite zimenezi chifukwa ali ndi mzimu woyera wa Mulungu. Iwo akufuna kukhala ndi ana amene angakhaledi anthu* a Mulungu. Choncho samalani kuti mukhale ndi maganizo oyenera ndipo musachitire zachinyengo akazi anu amene munawakwatira muli anyamata. 16 Chifukwa ine ndimadana ndi zoti anthu azithetsa mabanja,”+ watero Yehova Mulungu wa Isiraeli. “Ndimadana ndi munthu wankhanza.* Samalani kuti mukhale ndi maganizo oyenera ndipo musamachite zachinyengo,”+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.
17 “Inu mwatopetsa Yehova ndi mawu anu.+ Koma mukunena kuti, ‘Tamutopetsa bwanji?’ Ponena kuti, ‘Aliyense wochita zoipa ndi wabwino kwa Yehova ndipo amasangalala naye,’+ kapena ponena kuti, ‘Kodi Mulungu wachilungamo ali kuti?’”
3 “Taonani! Ine ndikutumiza mthenga wanga ndipo adzandikonzera njira.+ Mwadzidzidzi, Ambuye woona, amene anthu inu mukumufunafuna, adzabwera kukachisi wake.+ Ndiponso mthenga wa pangano amene mukumuyembekezera mosangalala adzabwera. Iye adzabwera ndithu,” watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.
2 “Ndani adzapirire pa tsiku limene adzabwere? Ndipo ndani adzaimirire iye akadzaonekera? Iye adzakhala ngati moto wa woyenga zitsulo komanso ngati sopo+ wa ochapa zovala. 3 Iye adzakhala pansi ngati woyenga zitsulo ndiponso ngati woyeretsa siliva.+ Adzayeretsa ana a Levi ndipo adzawayeretsa ngati golide ndi siliva. Akamadzapereka nsembe zawo ngati mphatso, Yehova adzaona kuti nsembe zawozo akuzipereka molungama. 4 Nsembe zimene Yuda ndi Yerusalemu adzapereke monga mphatso, zidzasangalatsa Yehova, ngati mmene zinalili kalekale ndiponso nthawi zamakedzana.+
5 Ndidzakuyandikirani kuti ndikuweruzeni. Sindidzazengereza kupereka umboni wotsutsa amatsenga,+ achigololo, olumbira monama+ komanso amene amachitira zachinyengo munthu waganyu,+ mkazi wamasiye ndi mwana wamasiye*+ komanso amene amakana kuthandiza alendo.+ Anthu amenewa sakundiopa,” watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.
6 “Ine ndine Yehova ndipo sindisintha.*+ Inu ndinu ana a Yakobo ndipo simunatheretu. 7 Kuyambira mʼmasiku a makolo anu mwakhala mukupatuka pa malamulo anga ndipo simunawatsatire.+ Bwererani kwa ine ndipo ine ndidzabwerera kwa inu,”+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.
Koma inu mukunena kuti: “Tingabwerere bwanji?”
8 “Kodi munthu wamba angabere Mulungu? Komatu inu mukundibera.”
Inu mukunena kuti: “Takuberani bwanji?”
“Mukundibera pa nkhani ya chakhumi ndi zopereka. 9 Ndinu otembereredwa* chifukwa mukundibera. Mtundu wanu wonsewu ukuchita zimenezi. 10 Bweretsani gawo limodzi pa magawo 10 alionse* a zinthu zanu nʼkuziika mosungiramo zinthu zanga,+ kuti mʼnyumba mwanga mukhale chakudya.+ Ndiyeseni chonde pa nkhani imeneyi, kuti muone ngati sindidzakutsegulirani mageti akumwamba+ nʼkukukhuthulirani madalitso mpaka simudzasowa kanthu,”+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.
11 “Ine sindidzalola kuti dzombe lizidzawononga mbewu zamʼmunda mwanu. Mitengo ya mpesa ya mʼmunda mwanu izidzabereka nthawi zonse,”+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.
12 “Mitundu ina yonse ya anthu idzanena kuti ndinu osangalala,+ chifukwa mudzakhala dziko losangalatsa,” watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.
13 “Inu mwandinenera mawu achipongwe,” watero Yehova.
Ndipo mukunena kuti: “Ife takunenerani zachipongwe zotani?”+
14 “Inu mwanena kuti, ‘Kutumikira Mulungu nʼkopanda phindu.+ Tapindula chiyani chifukwa chomutumikira ndiponso chifukwa choyenda mwachisoni pamaso pa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba? 15 Panopa tikuona kuti anthu odzikuza akusangalala. Komanso anthu ochita zoipa, zinthu zikuwayendera bwino.+ Iwo amayesa Mulungu koma sakulandira chilango.’”
16 Pa nthawi imeneyo anthu oopa Yehova ankalankhulana, aliyense ndi mnzake, ndipo Yehova anatchera khutu nʼkumamvetsera. Buku la chikumbutso, lonena za anthu oopa Yehova ndi anthu amene ankaganizira za dzina lake,* linayamba kulembedwa pamaso pake.+
17 “Iwo adzakhala anthu anga,+ pa tsiku limene ndidzawasandutse chuma chapadera,”+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. “Ndidzawachitira chifundo ngati mmene munthu amachitira chifundo mwana wake amene amamutumikira.+ 18 Ndipo mudzaonanso kusiyana pakati pa munthu wolungama ndi woipa+ ndiponso pakati pa munthu amene akutumikira Mulungu ndi amene sakumutumikira.”
4 “Taonani! Tsiku loyaka ngati ngʼanjo likubwera,+ ndipo anthu onse odzikuza ndi onse ochita zoipa adzakhala ngati mapesi. Pa tsikulo iwo adzawonongedwa moti sipadzatsala mizu kapena nthambi zawo,” watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. 2 “Koma inu amene mukulemekeza* dzina langa, dzuwa la chilungamo lidzakuwalirani ndipo kuwala kwake* kudzakhala ndi mphamvu yochiritsa. Mudzadumphadumpha ngati ana a ngʼombe amphongo onenepa.”
3 “Mudzapondaponda anthu oipa. Iwo adzakhala ngati fumbi kuphazi kwanu pa tsiku limene ndidzachitepo kanthu,” watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.
4 “Kumbukirani Chilamulo cha Mose mtumiki wanga. Kumbukirani malamulo ndi ziweruzo zomwe ndinamupatsa ku Horebe kuti Aisiraeli onse azitsatira.+
5 Tamverani! Tsiku la Yehova lalikulu ndi lochititsa mantha lisanafike,+ ndidzakutumizirani mneneri Eliya.+ 6 Iye adzachititsa mitima ya abambo kubwerera kwa ana awo+ ndi mitima ya ana kubwerera kwa abambo awo.* Adzachita zimenezi kuti ine ndisabwere kudzawononga dziko lapansi.”
(Malemba amene anawalemba mʼChiheberi ndi mʼChiaramu athera pamenepa. Malemba otsatirawa anawalemba mʼChigiriki.)
Kutanthauza “Mthenga Wanga.”
Kapena kuti, “ambuye wamkulu.”
Kapena kuti, “simundilemekeza.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mkate.”
Kapena kuti, “Kuchokera kumʼmawa mpaka kumadzulo.”
Mabaibulo ena amati, “mukundinyoza.”
Kutanthauza pamalo omwe ankatayapo ndowezo.
Kapena kuti, “malangizo.”
Mabaibulo ena amati, “malangizo anu.”
Mabaibulo ena amati, “malo opatulika.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amene ali maso ndiponso amene akuyankha.”
Kapena kuti, “amene munamukwatira mwalamulo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amene amaphimba zovala zake ndi chiwawa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mwana wopanda bambo.”
Kapena kuti, “sindinasinthe.”
Mabaibulo ena amati, “Mukunditemberera.”
Kapena kuti, “chakhumi chonse.”
Kapena kuti, “ankasinkhasinkha.” Mabaibulo ena amati, “ankaona kuti dzina lake ndi lamtengo wapatali.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mukuopa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmapiko mwake.”
Kapena kuti, “adzachititsa mitima ya abambo kuti ikhale ngati ya ana ndipo mitima ya ana kuti ikhale ngati ya abambo.”