4 Mmenemu munali chiwaya chagolide chofukizira nsembe,+ ndi likasa la pangano.+ Likasa lonseli linali lokutidwa ndi golide.+ M’likasamo munali mtsuko wagolide wokhala ndi mana.+ Munalinso ndodo ya Aroni imene inaphuka ija,+ komanso miyala yosema+ ya pangano.