-
2 Mbiri 13:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Iwo akufukiza nsembe zopsereza kwa Yehova m’mawa uliwonse ndi madzulo alionse.+ Akufukizanso mafuta onunkhira+ ndipo mikate yosanjikiza ili patebulo la golide woyenga bwino.+ Tilinso ndi choikapo nyale chagolide+ ndi nyale zake zimene amayatsa madzulo alionse.+ Tikuchita zimenezi chifukwa tikukwaniritsa udindo wathu+ kwa Yehova Mulungu wathu, koma inuyo mwamusiya.+
-
-
Numeri 16:40Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
40 Eleazara anachita izi kuti timalatato tikhale chikumbutso kwa ana a Isiraeli, kuti munthu aliyense amene si mbadwa+ ya Aroni asayandikire kwa Yehova+ kukafukiza nsembe. Anateronso kuti pasapezeke wina aliyense wochita zimene Kora limodzi ndi gulu lake+ anachita. Eleazara anachita zonse monga mmene Yehova anamuuzira kudzera kwa Mose.
-
-
1 Samueli 2:28Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
28 Kholo lakolo ndinalisankha kuchokera m’mafuko onse a Isiraeli kuti akhale wansembe wanga,+ ndipo azikwera paguwa langa lansembe+ kuti utsi wa nsembezo uzikwera kumwamba, kutinso azivala efodi pamaso panga. Ndinachita izi kuti ndipatse nyumba ya kholo lako nsembe zonse zotentha ndi moto za ana a Isiraeli.+
-