Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 9:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Ukakana, nditumiza miliri yanga yonse pa iwe, pa atumiki ako ndi anthu ako, kuti udziwe kuti palibe wofanana ndi ine padziko lonse lapansi.+

  • Ekisodo 15:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Ndi mulungu wina uti amene angafanane nanu, inu Yehova?+

      Ndinu woyera kopambana, ndani angafanane ndi inu?+

      Ndinu woyenera kuopedwa+ ndi kukuimbirani nyimbo zotamanda.+ Inu ndinu wochita zodabwitsa.+

  • 2 Samueli 7:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 N’chifukwa chake ndinudi wokwezeka,+ inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa. Ngakhale kuti tamva za milungu ina yambirimbiri, palibe Mulungu wina+ koma inu nokha.+

  • Salimo 83:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Kuti anthu adziwe+ kuti inu, amene dzina lanu ndinu Yehova,+

      Inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba,+ wolamulira dziko lonse lapansi.+

  • Salimo 86:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  8 Inu Yehova, palibe mulungu wina amene angafanane ndi inu.+

      Ndipo palibe ntchito zilizonse zofanana ndi ntchito zanu.+

  • Yesaya 46:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Kumbukirani zinthu zoyambirira zimene zinachitika kalekale,+ kuti ine ndine Mulungu+ ndipo palibenso Mulungu wina,+ kapena aliyense wofanana ndi ine.+

  • Yeremiya 10:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Ndithudi palibe aliyense wofanana ndi inu Yehova.+ Inu ndinu wamkulu, ndipo dzina lanu ndi lalikulu ndi lamphamvu.+

  • Aroma 9:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Pakuti ponena za Farao, Lemba linati: “Ndakusiya ndi moyo kuti ndikusonyeze mphamvu zanga, ndi kuti dzina langa lilengezedwe padziko lonse lapansi.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena