Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 8:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Pamenepo Farao anayankha kuti: “Mawa.” Ndiyeno Mose anati: “Zidzachitika monga mwa mawu anu, kuti mudziwe kuti palibenso wina wofanana ndi Yehova Mulungu wathu,+

  • Deuteronomo 33:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Palibe wina wofanana ndi Mulungu woona+ wa Yesuruni,+

      Amene amayenda m’mlengalenga pokuthandiza,+

      Amene amayenda pamitambo mu ulemerero wake.+

  • 2 Samueli 7:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 N’chifukwa chake ndinudi wokwezeka,+ inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa. Ngakhale kuti tamva za milungu ina yambirimbiri, palibe Mulungu wina+ koma inu nokha.+

  • Salimo 71:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Chilungamo chanu, inu Mulungu chafika kumwamba.+

      Tikanena za zinthu zazikulu zimene munachita,+

      Inu Mulungu, ndani angafanane ndi inu?+

  • Salimo 83:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Kuti anthu adziwe+ kuti inu, amene dzina lanu ndinu Yehova,+

      Inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba,+ wolamulira dziko lonse lapansi.+

  • Yesaya 45:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Ine ndine Yehova, ndipo palibenso wina.+ Palibenso Mulungu kupatulapo ine.+ Ndidzakumanga mwamphamvu m’chiuno mwako, ngakhale kuti sukundidziwa,

  • Yesaya 46:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Kumbukirani zinthu zoyambirira zimene zinachitika kalekale,+ kuti ine ndine Mulungu+ ndipo palibenso Mulungu wina,+ kapena aliyense wofanana ndi ine.+

  • Yeremiya 10:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Kodi ndani amene sangakuopeni,+ inu Mfumu ya mitundu yonse?+ Inuyo ndinu woyenera kuopedwa, chifukwa chakuti pakati pa anzeru onse a m’mitundu ya anthu ndiponso pakati pa maufumu awo onse, palibiretu aliyense wofanana ndi inu.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena