14 Ndiyeno amuna asanu amene anapita kukazonda+ dziko la Laisi+ aja, anauza abale awo kuti: “Kodi mukudziwa kuti m’nyumba izi muli efodi, aterafi,+ chifaniziro chosema+ ndi chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula?+ Ndiyetu dziwani chochita.”+