Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 18:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  6 Pa nthawi ya zowawa zanga ndinaitana Yehova,

      Ndinafuulira Mulungu wanga kuti andithandize.+

      Iye anamva mawu anga ali m’kachisi wake.+

      Pamenepo makutu ake anamva kulira kwanga kopempha thandizo.+

  • Salimo 27:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Yehova ndiye kuwala+ kwanga ndi chipulumutso changa.+

      Ndingaopenso ndani?+

      Yehova ndiye malo a chitetezo cha moyo wanga.+

      Ndingachitenso mantha ndi ndani?+

  • Salimo 31:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Ndathawira kwa inu Yehova.+

      Musalole kuti ndichite manyazi.+

      Ndipulumutseni chifukwa cha chilungamo chanu.+

  • Salimo 31:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  9 Ndikomereni mtima inu Yehova, pakuti ndasautsika kwambiri.+

      Diso langa lafooka chifukwa cha chisoni,+ chimodzimodzinso moyo wanga ndi m’mimba mwanga.+

  • Salimo 34:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Masoka a munthu wolungama ndi ochuluka,+

      Koma Yehova amamupulumutsa ku masoka onsewo.+

  • Salimo 43:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  5 N’chifukwa chiyani ukutaya mtima, moyo wangawe?+

      Ndipo n’chifukwa chiyani ukusautsika mkati mwanga?

      Yembekezera Mulungu,+

      Ndipo ndidzamutamanda pakuti iye ndiye mpulumutsi wanga wamkulu ndi Mulungu wanga.+

  • Salimo 56:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Popeza kuti ndine wogwirizana ndi Mulungu, ndidzatamanda mawu ake.+

      Ine ndimadalira Mulungu, sindidzaopa.+

      Kodi munthu angandichite chiyani?+

  • Salimo 143:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  5 Ndakumbukira masiku akale.+

      Ndasinkhasinkha zochita zanu zonse,+

      Ndipo ndakhala ndikuganizira ntchito ya manja anu ndi mtima wonse.+

  • Miyambo 18:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Dzina la Yehova ndi nsanja yolimba.+ Wolungama amathawira mmenemo ndipo amatetezedwa.+

  • Habakuku 3:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Ine ndidzakondwerabe mwa Yehova+ ndipo ndidzasangalala mwa Mulungu wachipulumutso changa.+

  • Luka 22:43
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 43 Pamenepo mngelo wochokera kumwamba anaonekera kwa iye ndi kumulimbikitsa.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena