Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 33:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Ndiwe wodala Isiraeli iwe!+

      Ndani angafanane ndi iwe,+

      Anthu amene akupulumutsidwa ndi Yehova,+

      Chishango chako chokuthandiza,+

      Amenenso ndi lupanga lako lopambana?+

      Adani ako adzakhala mwamantha chifukwa cha iwe,+

      Ndipo iwe udzayendayenda pamalo awo okwezeka.”+

  • Oweruza 2:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Yehova akawapatsa oweruza,+ Yehova anali kukhaladi ndi aliyense wa oweruzawo, ndipo iye anali kuwapulumutsa m’manja mwa adani awo masiku onse a moyo wa woweruzayo. Yehova anali kuchita zimenezo pakuti anali kuwamvera chisoni+ akamva kubuula kwawo chifukwa cha owapondereza ndi owakankhakankha.+

  • 2 Mafumu 19:34
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 34 Ndithu ndidzateteza+ mzinda uno kuti ndiupulumutse chifukwa cha ine mwini+ ndiponso chifukwa cha Davide mtumiki wanga.”’”+

  • Salimo 17:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  7 Sonyezani kukoma mtima kosatha mwa kuchita zodabwitsa,+ inu Mpulumutsi wa anthu othawira kwa inu,

      Amene akuthawa anthu ogalukira dzanja lanu lamanja.+

  • Salimo 44:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  7 Ndinu amene munatipulumutsa kwa adani athu,+

      Ndipo munanyazitsa anthu amene amadana nafe kwambiri.+

  • Yesaya 63:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Iye anati: “Ndithu awa ndi anthu anga,+ ana amene sadzachita zachinyengo.”+ Choncho iye anakhala Mpulumutsi wawo.+

  • Hoseya 1:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Koma ndidzachitira chifundo nyumba ya Yuda,+ ndipo Ine Yehova Mulungu wawo, ndidzawapulumutsa.+ Sindidzawapulumutsa ndi uta, lupanga, nkhondo, mahatchi* kapena ndi amuna okwera pamahatchi ayi.”+

  • 1 Timoteyo 4:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Pa chifukwa chimenechi, tikugwira ntchito mwakhama ndiponso mwamphamvu,+ chifukwa chiyembekezo+ chathu chili mwa Mulungu wamoyo, amene ali Mpulumutsi+ wa anthu a mtundu uliwonse,+ koma makamaka okhulupirika.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena