29 Munthu akakuukirani ndi kufunafuna moyo wanu, Yehova Mulungu+ adzakulunga ndi kuteteza moyo wanu m’phukusi la moyo+ monga mmene munthu amatetezera chuma chake. Koma moyo wa adani anu adzauponya ndi kuutaya kutali ngati mmene munthu amaponyera mwala ndi gulaye.*+