2 Samueli 21:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Kenako anaika mafupa a Sauli ndi Yonatani mwana wake m’dziko la Benjamini ku Zela+ m’manda a Kisi+ bambo ake, kuti achite zonse zimene mfumu inalamula. Izi zitachitika, Mulungu anamvetsera kuchonderera kwawo kuti amvere chisoni dziko lawo.+ 1 Mbiri 21:27 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 27 Kenako Yehova analankhula ndi mngelo uja,+ ndipo mngeloyo anabwezera lupanga lake m’chimake. 2 Mbiri 33:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Manase anayamba kupemphera kwa Mulungu ndipo iye anamva kupembedzera kwake+ ndi pempho lake lopempha chifundo. Kenako anam’bwezera ku Yerusalemu ku ufumu wake,+ ndipo Manase anadziwa kuti Yehova ndiye Mulungu woona.+ Yesaya 19:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Yehova adzakantha Iguputo.+ Adzamukantha n’kumuchiza,+ ndipo iwo adzabwerera kwa Yehova.+ Iye adzamva kuchonderera kwawo ndipo adzawachiritsa.+
14 Kenako anaika mafupa a Sauli ndi Yonatani mwana wake m’dziko la Benjamini ku Zela+ m’manda a Kisi+ bambo ake, kuti achite zonse zimene mfumu inalamula. Izi zitachitika, Mulungu anamvetsera kuchonderera kwawo kuti amvere chisoni dziko lawo.+
13 Manase anayamba kupemphera kwa Mulungu ndipo iye anamva kupembedzera kwake+ ndi pempho lake lopempha chifundo. Kenako anam’bwezera ku Yerusalemu ku ufumu wake,+ ndipo Manase anadziwa kuti Yehova ndiye Mulungu woona.+
22 Yehova adzakantha Iguputo.+ Adzamukantha n’kumuchiza,+ ndipo iwo adzabwerera kwa Yehova.+ Iye adzamva kuchonderera kwawo ndipo adzawachiritsa.+