Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 39:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 M’nyumba muno mulibe woyang’anira woposa ine, ndipo mbuye wanga anaika chilichonse m’manja mwanga kupatulapo inuyo, chifukwa ndinu mkazi wake.+ Ndiye ndingachitirenji choipa chachikulu chonchi n’kuchimwira Mulungu?”+

  • 1 Mafumu 15:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Anatero popeza Davide anachita zoyenera pamaso pa Yehova, ndipo sanapatuke pa chilichonse chimene Mulungu anamulamula masiku onse a moyo wake,+ kupatulapo pa nkhani ya Uriya Mhiti.+

  • 1 Mbiri 21:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Zinthu zimenezi zinali zoipa pamaso pa Mulungu woona,+ ndipo anapha Aisiraeli.

  • Salimo 5:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  6 Mudzawononga olankhula bodza.+

      Munthu wokhetsa magazi+ ndi wachinyengo,+ Yehova amaipidwa naye.

  • Salimo 11:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Yehova ali m’kachisi wake wopatulika.+

      Yehova, mpando wake wachifumu uli kumwamba.+

      Maso ake amaona, maso ake owala amasanthula+ ana a anthu.

  • Yeremiya 32:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Zolinga zanu ndi zazikulu+ ndipo zochita zanu ndi zambiri.+ Maso anu amaona njira zonse za ana a anthu+ kuti munthu aliyense mumuchitire zinthu mogwirizana ndi njira zake komanso zipatso za ntchito zake.+

  • Aheberi 4:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Palibe cholengedwa chimene Mulungu sangathe kuchiona.+ Chifukwa kwa iye zinthu zonse zili poonekera ndipo amatha kuziona bwinobwino. Ndipotu ife tikuyenera kudzayankha pa zochita zathu kwa Mulungu amene amaona zonseyo.+

  • Aheberi 13:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Ukwati ukhale wolemekezeka kwa onse, ndipo pogona pa anthu okwatirana pakhale posaipitsidwa,+ pakuti Mulungu adzaweruza adama ndi achigololo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena