Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 2:30
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 30 Koma Sihoni mfumu ya Hesiboni sanatilole kudutsa m’dziko lake, chifukwa Yehova Mulungu wanu anamulola kuti akhale wokanika+ ndi kuti aumitse mtima wake. Anatero kuti am’pereke m’manja mwanu monga mmene zilili lero.+

  • 2 Mbiri 10:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Mfumuyo sinamvere anthuwo chifukwa zinthu zinatembenuka chonchi mwa kufuna kwa Mulungu woona,+ kuti Yehova akwaniritse mawu ake+ amene analankhula kwa Yerobowamu mwana wa Nebati,+ kudzera mwa Ahiya+ Msilo.+

  • 2 Mbiri 22:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Koma Mulungu ndi amene anachititsa+ kuti Ahaziya awonongeke+ mwa kupita kwa Yehoramu. Atafika kumeneko, anatengana+ ndi Yehoramu n’kupita kukakumana ndi Yehu+ mdzukulu wa Nimusi,+ yemwe Yehova anam’dzoza+ kuti aphe a m’nyumba ya Ahabu.+

  • Salimo 5:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Mulungu adzawapeza ndi mlandu.+

      Adzagwa ndi ziwembu zawo zomwe.+

      Muwamwaze chifukwa cha kuchuluka kwa zolakwa zawo,+

      Chifukwa iwo akupandukirani.+

  • Miyambo 21:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Mtima wa mfumu uli ngati mitsinje yamadzi m’dzanja la Yehova.+ Amautembenuzira kulikonse kumene iye akufuna.+

  • Amosi 3:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Lipenga la nyanga ya nkhosa likalira mumzinda, kodi anthu sanjenjemera?+ Kodi tsoka likagwa mumzinda si Yehova amene wachititsa?

  • Aroma 9:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Chotero, iye amachitira chifundo munthu amene wafuna kumuchitira chifundo,+ koma amalola anthu ena kuti aumitse mitima yawo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena