Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 32:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Iwo andichititsa nsanje ndi milungu yachabe.+

      Andisautsa ndi mafano awo opanda pake.+

      Ndipo ine ndidzawachititsa nsanje ndi anthu achabe,+

      Ndidzawakhumudwitsa ndi mtundu wopusa.+

  • 1 Samueli 12:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Musapatuke kuti mutsatire milungu yopanda pake,+ yopanda phindu,+ imene singakulanditseni, pakuti ndi yopanda pake.

  • 2 Mafumu 17:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Iwo anapitiriza kukana malamulo ndi pangano+ limene iye anapangana ndi makolo awo, ndiponso zikumbutso+ zimene iye anali kuwachenjeza nazo. M’malomwake anayamba kutsatira mafano opanda pake+ ndipo iwowo nawonso anakhala opanda pake.+ Anatsatira mitundu imene inawazungulira, imene Yehova anawalamula kuti asamachite zofanana nayo.+

  • Yesaya 41:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Onsewo ali ngati chinthu choti kulibeko. Ntchito zawo si kanthu. Mafano awo opangidwa ndi zitsulo zosungunula ali ngati mphepo ndiponso zinthu zomwe si zenizeni.+

  • Yeremiya 10:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Munthu aliyense wachita zinthu mopanda nzeru kwambiri moti ndi zoonekeratu kuti sakudziwa kalikonse.+ Mmisiri wa zitsulo aliyense adzachita manyazi chifukwa cha chifaniziro chake chosula.+ Pakuti chifaniziro chake chopangidwa ndi chitsulo chosungunula ndi mulungu wonama+ ndipo mafano amenewa alibe moyo.+

  • Machitidwe 14:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 kuti: “Anthu inu, mukuchitiranji zimenezi? Ifenso ndife anthu+ okhala ndi zofooka+ ngati inu nomwe, ndipo tikulengeza uthenga wabwino kwa inu. Tikuchita izi kuti musiye zachabechabe zimenezi+ ndi kutembenukira kwa Mulungu wamoyo,+ amene anapanga kumwamba,+ dziko lapansi, nyanja ndi zonse zokhala mmenemo.

  • Aroma 1:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 ndipo anasandutsa ulemerero+ wa Mulungu amene sawonongeka kukhala ngati chifaniziro+ cha munthu, mbalame, zolengedwa za miyendo inayi ndi zokwawa,+ zonsezo zimene zimawonongeka.

  • 1 Akorinto 8:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Ndiyeno pa nkhani ya kudya+ zakudya zoperekedwa kwa mafano, timadziwa kuti fano ndi lopanda pake+ m’dziko, ndiponso kuti kulibe Mulungu wina koma mmodzi yekha.+

  • 1 Akorinto 10:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Ndiye ndinene chiyani? Kuti choperekedwa nsembe kwa fano chili kanthu, kapena kuti fanolo ndi kanthu?+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena