4 Choncho Ahabu analowa m’nyumba mwake ali wachisoni ndi wokhumudwa chifukwa cha mawu amene Naboti Myezereeli anamuuza, onena kuti: “Sindikupatsani cholowa cha makolo anga.” Ndiyeno anakagona pabedi lake n’kutembenukira kukhoma,+ ndipo sanadye chakudya.