9 Koma Sauli ndi anthu ake anamvera chisoni Agagi ndipo sanaphe nkhosa ndi ng’ombe zabwino kwambiri,+ ziweto zonenepa, nkhosa zamphongo ndi zina zonse zimene zinali zabwino. Iwo sanafune kupha zimenezi,+ koma anawononga zinthu zina zonse zimene zinali zonyansa ndi zonyozeka.