-
1 Mafumu 12:32Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
32 M’mwezi wa 8, pa tsiku la 15 la mweziwo, Yerobowamu anachita chikondwerero chofanana ndi cha ku Yuda.+ Anachita chikondwererochi kuti apereke nsembe kwa ana a ng’ombe amene anawapanga, paguwa lansembe limene analimanga ku Beteli.+ M’malo okwezeka a ku Beteli amene anamanga, anaikako ansembe kuti azitumikira.
-
-
1 Mafumu 14:10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Pa chifukwa chimenechi, ndibweretsa tsoka panyumba ya Yerobowamu. Ndithu ndidzapha munthu aliyense wokodzera khoma*+ wa m’nyumba ya Yerobowamu, ngakhale anthu onyozeka ndi opanda pake mu Isiraeli.+ Komanso ndidzaseseratu nyumba ya Yerobowamu,+ monga momwe munthu amasesera ndowe mpaka atakazitaya.+
-
-
2 Mbiri 13:3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Choncho Abiya anapita kukamenya nkhondoyo ndi gulu la amuna amphamvu ankhondo+ osankhidwa mwapadera okwanira 400,000. Yerobowamu nayenso anapita kukamenyana ndi Abiya ndipo anapita ndi asilikali 800,000. Amenewa anali amuna amphamvu ndi olimba mtima osankhidwa mwapadera, ndipo anakafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo.+
-