21Tsopano m’masiku a Davide kunagwa njala+ zaka zitatu zotsatizana. Choncho Davide anafunsira kwa Yehova, ndipo Yehova anamuuza kuti: “Sauli pamodzi ndi nyumba yake ali ndi mlandu wa magazi chifukwa anapha Agibeoni.”+
17Eliya+ wa ku Tisibe, wochokera ku Giliyadi+ analankhula ndi Ahabu kuti: “Pali Yehova Mulungu wamoyo, Mulungu wa Isiraeli+ amene ndimam’tumikira,+ sikugwa mame kapena mvula+ zaka zikubwerazi, pokhapokha ine nditalamula.”+