Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 35:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Atatero anachoka, ndipo anthu a m’mizinda yowazungulira anagwidwa ndi mantha ochokera kwa Mulungu,+ moti sanatsatire ana a Yakobo kuti akawathire nkhondo.

  • Ekisodo 15:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Adzaopa ndipo adzagwidwa ndi mantha aakulu.+

      Chifukwa cha dzanja lanu lamphamvu, adzakhala chete ngati mwala.

      Kufikira anthu anu+ atadutsa, inu Yehova,

      Kufikira anthu anu amene munawapanga+ atadutsa.+

  • Deuteronomo 11:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Palibe munthu amene adzaima kuti alimbane nanu.+ Yehova Mulungu wanu adzachititsa dziko lonse limene mudzapondapo kugwidwa ndi mantha aakulu ndi kukuopani,+ monga mmene anakulonjezerani.

  • Yoswa 5:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Mafumu onse a Aamori+ amene anali kutsidya la kumadzulo kwa mtsinje wa Yorodano, ndi mafumu onse a Akanani+ amene anali m’mphepete mwa nyanja, anamva zakuti Yehova anaphwetsa madzi a mtsinje wa Yorodano pamaso pa ana a Isiraeli kufikira atawoloka. Atamva zimenezo, mitima yawo inasungunuka ndi mantha,+ moti anatheratu mphamvu poopa ana a Isiraeli.+

  • 2 Mbiri 17:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Mantha+ ochokera kwa Yehova anagwira maufumu onse a m’mayiko ozungulira Yuda, ndipo sanachite nkhondo ndi Yehosafati.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena