23 Ndiyeno Mose atakhala kumeneko nthawi yaitali, mfumu ya Iguputo inamwalira.+ Koma ana a Isiraeli anapitirizabe kuvutika ndi ukapolo ndi kulira modandaula.+ Iwo anapitirizabe kulirira thandizo kwa Mulungu woona chifukwa cha ukapolowo.+
10 Farao atafika pafupi, ana a Isiraeli anakweza maso awo ndipo anaona Aiguputo akuwathamangira. Pamenepo ana a Isiraeli anachita mantha kwambiri ndipo anayamba kufuulira Yehova.+