Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 75:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  8 M’dzanja la Yehova muli kapu.+

      Kapuyo yadzaza ndi vinyo wosakaniza ndi zokometsera ndipo akuchita thovu.

      Ndithudi, iye adzatsanula vinyo yense amene ali m’kapuyo kuphatikizapo nsenga zake.

      Anthu onse oipa padziko lapansi adzamwa ndi kugugudiza nsengazo.”+

  • Yesaya 51:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 “Dzuka! Dzuka! Imirira iwe Yerusalemu,+ iwe amene wamwa chikho cha mkwiyo wa Yehova kuchokera m’dzanja lake.+ Iweyo wamwa ndipo wagugudiza chipanda, chikho chochititsa munthu kuyenda dzandidzandi.+

  • Yeremiya 25:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Yehova Mulungu wa Isiraeli anandiuza kuti: “Landira chikho ichi chimene chili m’dzanja langa. Mmenemu muli vinyo wa mkwiyo ndipo ukamwetse mitundu yonse imene ndikukutumizako.+

  • Habakuku 2:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Iwenso adzakumwetsa+ ndipo udzaonekera kuti ndiwe wosadulidwa.+ Udzakhuta zinthu zamanyazi m’malo mwa ulemerero.+ Chikho chochokera m’dzanja lamanja la Yehova chidzakupeza+ ndipo ulemerero wako udzasanduka manyazi.

  • Chivumbulutso 16:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Pamenepo mzinda waukulu+ unagawika zigawo zitatu, ndipo mizinda ya mitundu ya anthu inagwa. Ndiyeno Mulungu anakumbukira Babulo Wamkulu,+ kuti amupatse kapu yokhala ndi vinyo wa mkwiyo wake waukulu.+

  • Chivumbulutso 18:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 M’bwezereni monga mmene iye anachitira.+ M’chitireni mowirikiza kawiri. Ndithu, wirikizani kawiri zinthu zimene iyeyo anachita.+ M’kapu+ imene anaikamo chakumwa chosakaniza, ikanimo chakumwa chakecho+ kuwirikiza kawiri.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena