Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 6:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 “Tamverani, Aisiraeli inu: Yehova Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi.*+

  • Deuteronomo 32:39
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 39 Onani tsopano kuti ndine Mulungu,+

      Ndipo palibe milungu ina pamodzi ndi ine.+

      Ndimapha ndiponso ndimapereka moyo.+

      Ndavulaza koopsa,+ ndipo ine ndidzachiritsa,+

      Palibe aliyense wonditsomphola m’dzanja langa.+

  • Salimo 83:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Kuti anthu adziwe+ kuti inu, amene dzina lanu ndinu Yehova,+

      Inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba,+ wolamulira dziko lonse lapansi.+

  • Yesaya 37:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 “Inu Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli+ wokhala pa akerubi, inu nokha ndinu Mulungu woona wa maufumu onse a padziko lapansi.+ Inuyo munapanga kumwamba ndi dziko lapansi.+

  • Yesaya 44:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 “Yehova, Mfumu ya Isiraeli,+ Womuwombola iye,+ Yehova wa makamu, wanena kuti: ‘Ine ndine woyamba ndi womaliza,+ ndipo palibenso Mulungu kupatulapo ine.+

  • Maliko 12:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Yesu anayankha kuti: “Loyamba n’lakuti, ‘Tamverani Aisiraeli inu, Yehova* Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi.+

  • 1 Akorinto 8:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Ndiyeno pa nkhani ya kudya+ zakudya zoperekedwa kwa mafano, timadziwa kuti fano ndi lopanda pake+ m’dziko, ndiponso kuti kulibe Mulungu wina koma mmodzi yekha.+

  • Aefeso 4:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 ndi Mulungu mmodzi+ amenenso ndi Atate wa anthu onse. Iye ali pamwamba pa onse ndipo amachita zinthu kudzera mwa onse ndiponso mphamvu yake imagwira ntchito mwa onse.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena