Salimo 36:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Inu Mulungu, kukoma mtima kwanu kosatha ndi kwamtengo wapatali!+Ndipo ana a anthu amabisala mu mthunzi wa mapiko anu.+ Salimo 51:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 51 Ndikomereni mtima inu Mulungu, malinga ndi kukoma mtima kwanu kosatha.+Malinga ndi kuchuluka kwa chifundo chanu, fafanizani zolakwa zanga.+ Salimo 63:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Pakuti kukoma mtima kwanu kosatha n’kwabwino kuposa moyo,+Milomo yanga idzakuyamikirani.+ Salimo 85:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Inu Yehova, tisonyezeni kukoma mtima kwanu kosatha,+Ndipo tipatseni chipulumutso chanu.+
7 Inu Mulungu, kukoma mtima kwanu kosatha ndi kwamtengo wapatali!+Ndipo ana a anthu amabisala mu mthunzi wa mapiko anu.+
51 Ndikomereni mtima inu Mulungu, malinga ndi kukoma mtima kwanu kosatha.+Malinga ndi kuchuluka kwa chifundo chanu, fafanizani zolakwa zanga.+