1 Samueli 16:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Mmodzi mwa atumikiwo anayankha, kuti: “Inetu ndinaona luso loimba+ la mwana wa Jese wa ku Betelehemu. Iye ndi mwamuna wolimba mtima ndiponso wamphamvu,+ mwamuna wankhondo,+ wolankhula mwanzeru+ ndi wooneka bwino,+ komanso Yehova ali naye.”+ 2 Samueli 16:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Ndiyeno masiku amenewo munthu akalandira malangizo kwa Ahitofeli, zinali ngati kuti munthu wafunsira malangizo kwa Mulungu woona. Umu ndi mmene malangizo+ onse a Ahitofeli+ analili, kwa Davide ndi Abisalomu yemwe. 1 Mafumu 7:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Mayi ake anali mkazi wamasiye wa fuko la Nafitali. Bambo ake anali a ku Turo+ odziwa kupanga zinthu ndi mkuwa.+ Hiramu anali wanzeru, womvetsa bwino zinthu,+ ndiponso wodziwa bwino kupanga zinthu zosiyanasiyana zamkuwa. Iye anabwera kwa Mfumu Solomo n’kuyamba kumugwirira ntchito yake yonse. Danieli 1:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 Pamenepo mfumu inayamba kulankhula nawo ndipo pa ana onsewo, palibe aliyense amene anali ngati Danieli, Hananiya, Misayeli ndi Azariya.+ Chotero ana amenewa anapitiriza kutumikira mfumu.+
18 Mmodzi mwa atumikiwo anayankha, kuti: “Inetu ndinaona luso loimba+ la mwana wa Jese wa ku Betelehemu. Iye ndi mwamuna wolimba mtima ndiponso wamphamvu,+ mwamuna wankhondo,+ wolankhula mwanzeru+ ndi wooneka bwino,+ komanso Yehova ali naye.”+
23 Ndiyeno masiku amenewo munthu akalandira malangizo kwa Ahitofeli, zinali ngati kuti munthu wafunsira malangizo kwa Mulungu woona. Umu ndi mmene malangizo+ onse a Ahitofeli+ analili, kwa Davide ndi Abisalomu yemwe.
14 Mayi ake anali mkazi wamasiye wa fuko la Nafitali. Bambo ake anali a ku Turo+ odziwa kupanga zinthu ndi mkuwa.+ Hiramu anali wanzeru, womvetsa bwino zinthu,+ ndiponso wodziwa bwino kupanga zinthu zosiyanasiyana zamkuwa. Iye anabwera kwa Mfumu Solomo n’kuyamba kumugwirira ntchito yake yonse.
19 Pamenepo mfumu inayamba kulankhula nawo ndipo pa ana onsewo, palibe aliyense amene anali ngati Danieli, Hananiya, Misayeli ndi Azariya.+ Chotero ana amenewa anapitiriza kutumikira mfumu.+