-
2 Mbiri 32:15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Tsopano musalole kuti Hezekiya akupusitseni+ kapena kukunyengererani+ chonchi ndipo musamukhulupirire, chifukwa palibe ufumu uliwonse kapena mulungu wa mtundu uliwonse wa anthu amene anatha kupulumutsa anthu akewo m’manja mwanga ndiponso m’manja mwa makolo anga. Ndiye mukuganiza kuti Mulungu wanu angakupulumutseni m’manja mwanga?’”+
-
-
Salimo 2:2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Mafumu a dziko lapansi aima pamalo awo,+
Ndipo nduna zapamwamba zasonkhana pamodzi mogwirizana.+
Atero kuti alimbane ndi Yehova+ komanso wodzozedwa wake.+
-
Danieli 3:15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Tsopano ngati mwakonzeka kuti mukamva kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze wamng’ono, zoimbira zosiyanasiyana za zingwe, chitoliro chathumba ndi zipangizo zosiyanasiyana zoimbira,+ mugwada n’kuwerama mpaka nkhope zanu pansi ndi kulambira fano lagolide, zili bwino. Koma ngati simulilambira, nthawi yomweyo muponyedwa m’ng’anjo yoyaka moto. Ndipo ndi mulungu uti amene angakupulumutseni m’manja mwanga?”+
-
-
-