Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 32:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Pamenepo iye analandira golideyo kuchokera kwa anthuwo ndipo pogwiritsa ntchito chosemera, anam’panga+ kukhala fano la mwana wa ng’ombe+ lopangidwa ndi golide wosungunula. Zitatero iwo anayamba kunena kuti: “Uyu ndiye Mulungu wanu, Aisiraeli inu, amene anakutulutsani m’dziko la Iguputo.”+

  • Salimo 97:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  7 Onse amene akupembedza chifaniziro chilichonse achite manyazi.+

      Amene amadzitama chifukwa cha milungu yopanda pake achite manyazi.+

      Muweramireni, inu milungu yonse.+

  • Yesaya 1:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Pakuti anthu adzachita manyazi ndi mitengo ikuluikulu imene inu munali kuilakalaka,+ ndipo mudzagwetsa nkhope zanu chifukwa cha minda imene mwasankha.+

  • Yesaya 44:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Anzake onse adzachita manyazi,+ ndipotu amisiriwo ndi anthu ochokera kufumbi. Onsewo adzasonkhana pamodzi.+ Adzaima chilili. Adzachita mantha. Onsewo adzachitira limodzi manyazi.+

  • Yesaya 44:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Koma mtengo wotsalawo wapangira mulungu, wapangira chifaniziro chake chosema. Wachiweramira ndi kuchigwadira n’kumapemphera pamaso pake kuti: “Ndipulumutseni, pakuti ndinu mulungu wanga.”+

  • Yesaya 45:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Anthu adzachita manyazi ndipo onsewo adzanyozeka. Anthu opanga mafano adzayenda monyozeka onse pamodzi.+

  • Yeremiya 2:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 “Monga mmene mbala imachitira manyazi ikagwidwa, anthu a m’nyumba ya Isiraeli nawonso achita manyazi,+ iwowo, mafumu awo, akalonga awo, ansembe awo ndiponso aneneri awo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena