Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mbiri 36:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Choncho anawabweretsera mfumu ya Akasidi+ yomwe inapha anyamata awo ndi lupanga+ m’nyumba yopatulika.+ Sinachitire chisoni mnyamata kapena namwali, wachikulire kapena nkhalamba yotheratu.+ Mulungu anapereka zonse m’manja mwake.

  • Yesaya 49:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Koma Ziyoni ankangonena kuti: “Yehova wandisiya+ ndipo Yehova wandiiwala.”+

  • Yeremiya 30:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 “Ndidzakubwezeretsa mwakale ndipo ndidzachiritsa zilonda zako za mkwapulo,”+ watero Yehova. “Iwo anakutcha kuti mkazi wothamangitsidwa ndipo anali kunena kuti:+ ‘Ameneyu ndi Ziyoni ndipo palibe amene akumufunafuna.’”+

  • Yeremiya 33:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 “Yehova wanena kuti, ‘Anthu inu mudzanena za dziko lino kuti ndi lopanda pake chifukwa mulibe anthu ndi ziweto. Mudzanena zimenezi za mizinda ya Yuda ndi misewu ya Yerusalemu imene yawonongeka,+ moti mulibe anthu ndipo simukukhala munthu aliyense ngakhale ziweto.+

  • Maliro 1:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Njira zopita ku Ziyoni zikulira, chifukwa palibe amene akupita kuchikondwerero.+

      Zipata zake zonse zasiyidwa.+ Ansembe+ ake akuusa moyo.*

      Anamwali ake agwidwa ndi chisoni,+ ndipo iyeyo akumva kuwawa mumtima.

  • Agalatiya 4:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Pakuti Malemba amati: “Kondwera, mkazi wosabereka iwe amene sunaberekepo mwana. Kuwa ndipo fuula mokondwa, iwe mkazi amene sunamvepo zowawa za pobereka, pakuti ana a mkazi wosiyidwa ndi ambiri kuposa ana a mkazi amene ali ndi mwamuna.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena