12 Inu a m’nyumba ya Davide,+ Yehova wanena kuti: “M’mawa uliwonse+ muziweruza mwachilungamo,+ ndipo muzilanditsa munthu kwa anthu achinyengo amene akufuna kumulanda katundu.+ Muzitero kuti mkwiyo wanga usayake ngati moto+ ndi kukutenthani popanda wouzimitsa chifukwa cha kuipa kwa zochita zanu.”’+