Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 28:63
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 63 “Chotero, monga mmene Yehova anasangalalira kuti akuchitireni zabwino ndi kukuchulukitsani,+ momwemonso adzasangalala kuti akuwonongeni ndi kukufafanizani.+ Pamenepo mudzatheratu m’dziko limene mukupita kukalitenga kukhala lanu.+

  • Yesaya 1:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Dziko lanu lawonongedwa.+ Mizinda yanu yatenthedwa ndi moto,+ ndipo alendo akudya zokolola zochokera munthaka yanu, inu mukuona.+ Chilichonse chawonongeka ngati mmene zimakhalira adani akalanda dziko.+

  • Yesaya 5:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Tsopano amuna inu, ndikuuzani zimene ndichite ndi munda wanga wa mpesa: Ndichotsa zomera zimene zinali ngati mpanda wa mundawo,+ ndipo ndiutentha.+ Ndigumula mpanda wake wamiyala ndipo mundawo udzangokhala malo oti azipondapondapo.+

  • Yeremiya 4:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Kwezani chizindikiro choloza njira ya ku Ziyoni. Thawirani kumalo otetezeka. Musaime chilili.” Chitani zimenezi chifukwa ndikubweretsa tsoka kuchokera kumpoto,+ ndithu ndikubweretsa tsoka lalikulu.

  • Ezekieli 6:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 M’malo anu onse okhala,+ mizinda idzawonongedwa+ ndipo malo okwezeka adzasakazidwa kuti akhale mabwinja ndiponso kuti maguwa anu ansembe akhale osakazidwa.+ Chotero maguwa anu ansembewo adzaphwanyidwa+ ndipo mafano anu onyansa sadzakhalaponso.+ Maguwa anu ofukizirapo zonunkhira adzagwetsedwa+ ndipo ntchito za manja anu zidzafafanizidwa.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena