Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ezara 3:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Ansembe+ ndi Alevi ambiri, omwe anali atsogoleri a nyumba za makolo awo,+ amuna okalamba amene anaona nyumba yoyambirira,+ anali kulira+ mokweza chifukwa cha kumangidwa kwa maziko+ a nyumbayo pamaso pawo, ndipo enanso ambiri anali kufuula mosangalala.+

  • Nehemiya 8:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Choncho mpingo wonse wa anthu amene anabwerera kuchokera ku ukapolo anamanga misasa ndi kukhala m’misasayo. Panali chisangalalo chachikulu kwambiri+ chifukwa chakuti ana a Isiraeli anali asanachitepo zimenezi kuchokera m’masiku a Yoswa mwana wa Nuni,+ mpaka kudzafika tsiku limeneli.

  • Yesaya 35:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Anthu owomboledwa ndi Yehova adzabwerera+ n’kukafika ku Ziyoni akufuula mosangalala.+ Iwo azidzasangalala mpaka kalekale.+ Adzakhala okondwa ndi osangalala ndipo chisoni ndi kubuula zidzachoka.+

  • Yesaya 51:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Chotero, owomboledwa a Yehova adzabwerera ku Ziyoni ndi mfuu yachisangalalo,+ ndipo pamutu pawo padzakhala chisangalalo mpaka kalekale.+ Iwo adzapeza chisangalalo ndi chimwemwe.+ Chisoni ndi kuusa moyo zidzachoka.+

  • Yeremiya 31:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Chotero ndidzakumanganso ndipo udzakhazikika,+ iwe namwali wa Isiraeli. Udzanyamula maseche ndi kupita kukavina pamodzi ndi anthu amene akuseka.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena