9 “Yehova wanena kuti, ‘Popeza kuti Turo+ anapanduka mobwerezabwereza, sindidzamusinthira chigamulo changa. Sindidzamusinthira chigamulocho chifukwa chakuti anapereka ku Edomu gulu lonse la anthu ogwidwa ukapolo, ndiponso chifukwa chakuti sanakumbukire pangano la pa ubale.+